Yakobo 2:9-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. koma ngati musamala maonekedwe, mucita ucimo, ndipo mutsutsidwa ndi cilamulo monga olakwa.

10. Pakuti amene ali yense angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wacimwira onse.

11. Pakuti Iye wakuti, Usacite cigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kucita cigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo.

Yakobo 2