Oweruza 7:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndi kuwerenga kwa iwo akukhatira, ndi kuika dzanja lao kukamwa kwao, ndiko mazana atatu; koma ena onse anagwada pakumwa madzi.

7. Ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ndi anthu mazana atatu akukhatira ndidzakupulumutsani, ndi kupereka Amidyani m'dzanja lako; koma amuke anthu awa onse, yense kumalo kwace.

8. Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israyeli amuke, yense kuhema kwace; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midyani inali kunsi kwace m'cigwa.

9. Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako.

10. Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa;

11. nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wace ku cilekezero ca anthu azidaa m'misasa.

12. Ndipo Amidyani ndi Aamaleki ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'cigwa, kucuruka kwao ngati dzombe; ndi ngamila zao zosawerengeka, kucuruka kwao ngati mcenga wa m'mphepete mwa nyanja.

Oweruza 7