Oweruza 7:24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Gideoni anatumanso mithenga ku mapiri onse a Efraimu ndi kuti, Tsikani, kukomana ndi Amidyani ndi kutsekereza madooko asanafike iwowa, mpaka ku Beti-bara ndi Yordano. Potero amuna onse a Efraimu anasonkhana pamodzi natsekereza madooko mpaka ku Betibara, ndi Yordano.

Oweruza 7

Oweruza 7:21-25