6. Ndipo Israyeli anafoka kwambiri cifukwa ca Midyani; ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova.
7. Ndipo kunali, pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova cifukwa ca Midyani,
8. Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israyeli, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ine ndinakukwezani kucokera m'Aigupto, ndi kukuturutsani m'nyumba ya ukapolo;
9. ndipo ndinakulanditsani m'dzanja la Aaigupto, ndi m'dzanja la onse akupsinja inu, ndi kuwaingitsa pamaso panu, ndi kukupatsani dziko lao;
10. ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvera mau anga.
11. Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala m'Ofira, wa Yoasi M-abieziri; ndi mwana wace Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidyani.
12. Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe.