1. Ndipo ana a Israyeli anaonjeza kucita coipa pamaso pa Yehova, atafa Ehudi.
2. Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wocita ufumu ku Hazori; kazembe wace wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu.
3. Ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova; pakuti anali nao magareta acitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israyeli kolimba zaka makumi awiri.