22. Atafika kutari ndi nyumba ya Mika, Mikayo anawamemeza amuna a m'nyumba zoyandikizana ndi yace, natsata ndi kuwapeza ana a Dani.
23. Ndipo anapfuula kwa ana a Dani. Naceuka iwo nati kwa Mika, Cakusowa ciani, kuti wamemeza anthu ako?
24. Nati iye, Mwanditengera milungu yanga ndinaipanga, ndi wansembe, ndi kucoka; cinditsaliranso ciani? ndipo muneneranji kwa ine, Cakusowa nciani?
25. Koma ana a Dani anati kwa iye, Mau ako asamveke ndi ife, angakugwere anthu owawa mtima, nukataya moyo wako ndi wa iwo a m'nyumba mwako.