Pamenepo Mulungu anang'amba pokumbika paja pit Leki, naturukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wace, natsitsimuka iye; cifukwa cace anawacha dzina lace, Kasupe wa wopfuula, ndiwo m'Leki mpaka lero lino.