Oweruza 15:17-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo kunali, atatha kunena, anataya cibwano m'dzanja lace; nawacha maiowo Ramati-leki ndiko kunena citunda ca cibwano.

18. Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu cipulumutso ici cacikuru ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa?

19. Pamenepo Mulungu anang'amba pokumbika paja pit Leki, naturukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wace, natsitsimuka iye; cifukwa cace anawacha dzina lace, Kasupe wa wopfuula, ndiwo m'Leki mpaka lero lino.

20. Ndipo Samsoni anaweruza Israyeli m'masiku a Afilisti zaka makumi awiri.

Oweruza 15