Pamene anafika ku Leki Afilisti anapfuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ace zinanga bwazi lopserera ndi moto, ndi zomangira zace zinanyotsoka pa manja ace.