1. Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kuceka tirigu Samsoni anakaceza ndi mkazi wace ndi kumtengera mbuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kucipinda. Koma atate wace sanamlola kulowamo.
2. Nati atate wace, Ndinanenetsa kuti umuda konse, potero ndinampereka kwa bwenzi tako; mng'ono wace sakoma koposa iye nanga? ukhale naye, m'malo mwa winayu.
3. Koma Samsoni ananena nao, Nthawi yino ndikhala wosaparamula pa Afilisti, powacitira coipa ine.
4. Namuka Samsoni, nagwira ankhandwe mazana atatu, natenga miuni, nalunza micira, naika muuni pakati pa micira iwiri iri yonse.
5. Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosaceka wa Afilisti, natentha miulu ndi tirigu wosaceka yemwe, ndi minda ya azitona yomwe.