Oweruza 13:2-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lace ndiye Manowa; ndi mkazi wace analibe mwana, sanabala.

3. Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana, wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.

4. Cifukwa cace udzisamalire, usamwe vinyo kapena coledzeretsa, nusadye cinthu ciri conse codetsa;

5. pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pace sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israyeli m'dzanja la Afilisti.

6. Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wace ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ace ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunsa uko acokera kapena sanandiuzanso dzina lace;

7. koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena coledzeretsa, nusadye ciri conse codetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire mpaka tsiku la kufa kwace.

Oweruza 13