Oweruza 13:15-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Tiloleni tikucedwetseni kuti tikukonzereni mwana wa mbuzi.

16. Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undicedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwa kuti ndiye mthenga wa Yehova.

17. Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Dzina lanu ndani, kuti, atacitika mau anu, tikucitireni ulemu.

18. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ufunsiranji dzina langa, popeza liri lodabwitsa?

19. Pamenepo Manowa anatenga mwana wa mbuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anacita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wace ali cipenyereo

Oweruza 13