Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undicedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwa kuti ndiye mthenga wa Yehova.