Oweruza 12:4-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Gileadi nalimbana naye Efraimu; ndipo amuna a Gileadi anakantha Efraimu, cifukwa adati, Inu Agileadi ndinu akuthawa Efraimu, pakati pa Efraimu ndi pakati pa Manase.

5. Ndipo Agileadi anatsekereza madooko a Yordano a Efraimu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efraimu, Ndioloke, amuna a Gileadi anati kwa iye, Ndiwe M-efraimu kodi? Akati, Iai;

6. pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kuchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordano; ndipo anagwa a Efraimu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri.

7. Ndipo Yefita anaweruza Israyeli zaka zisanu ndi cimodzi; nafa Yefita Mgileadi, naikidwa m'mudzi wina wa Gileadi.

8. Ndi pambuyo pace Ibzani wa ku Betelehemu anaweruza Israyeli.

Oweruza 12