16. Pamenepo anacotsa milungu yacilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wace unagwidwa cisoni cifukwa ca mabvuto a Israyeli.
17. Ndipo ana a Amoni analalikiridwa, namanga misasa m'Gileadi. Ndi ana a Israyeli anasonkhana namanga misasa ku Mizipa.
18. Ndipo anthu, akalonga a Gileadi, ananenana wina ndi mnzace, Ndaniyo adzayamba kulimbana ndi ana a Amoni? iye adzakhala mkuru wa onse okhala m'Gileadi.