Nyimbo 8:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwenzi utakhala ngati mlongwanga,Woyamwa pa bere la amai!Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona;Osandinyoza munthu.

2. Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai,Kuti andilange mwambo; Ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa,Ndi madzi a makangaza anga.

3. Dzanja lamanzere lace akadanditsamiritsa kumutu,Lamanja lace ndi kundifungatira.

Nyimbo 8