Numeri 9:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakacitira Yehova Paskha, azicita monga mwa lemba la Paskha, ndi monga mwa ciweruzo cace; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.

15. Ndipo tsiku loutsa kacisi mtambo unaphimba kacisi, ndiwo cihema cokomanako; ndipo madzulo padaoneka pakacisi ngati moto, kufikira m'mawa.

16. Kudatero kosalekeza; mtambo umaciphimba, ndimoto umaoneka usiku,

17. Ndipo pokwera mtambo kucokera kucihema, utatero ana a Israyeli amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israyeli amamanga mahema ao.

18. Pakuwauza Yehova ana a Israyeli amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa kacisi amakhala m'cigono.

19. Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa kacisi, pamenepo ana a Israyeli anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo.

20. Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa kacisi masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'cigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.

Numeri 9