12. Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yaucimo, ndi inzace, nsembe yopsereza za Yehova, kucita cotetezera Alevi.
13. Ndipo uimike Alevi pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ace, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula kwa Yehova.
14. Momwemo upatule Alevi mwa ana a Israyeli; kuti Alevi akhale anga.
15. Ndipo atatero alowe Alevi kucita Debito ya cihema cokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula.
16. Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ocokera mwa ana a Israyeli; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula m'mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israyeli.