Numeri 7:49-59 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

49. copereka cace mbizi Imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

50. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

51. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

52. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

53. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa za mphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Elisama mwana wa Amihudi.

54. Tsiku lacisanu ndi citatu kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliyeli mwana wa Pedazuri:

55. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

56. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

57. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

58. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

59. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.

Numeri 7