Numeri 36:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israyeli dzikoli mocita maere likhale colowa cao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ace akazi colowa ca Tselofekadi mbale wathu.

3. Ndipo akakwatibwa nao ana amuna a mapfuko ena a ana a Israyeli, acicotse colowa cao ku colowa ca makolo athu, nacionjeze ku colowa ca pfuko limene adzakhalako; cotero acicotse ku maere a colowa cathu.

4. Ndipo pofika caka coliza ca ana a Israyeli adzaphatikiza colowa cao ku colowa ca pfuko limene akhalako; cotero adzacotsa colowa cao ku colowa ca pfuko la makolo athu.

5. Ndipo Mose analamulira ana a Israyeli monga mwa mau a Yehova, nati, Pfuko la ana a Yosefe linena zaona.

6. Colamulira Yehova za ana akazi a Tselofekadi ndi ici, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ace; komatu akwatibwe nao a banja la pfuko la makolo ao okha okha.

Numeri 36