9. Ndipo ana a Israyeli anagwira akazi a Amidyani, ndi ana ang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi cuma cao conse.
10. Ndipo anatentha ndi moto midzi yao yonse yokhalamo iwo, ndi zigono zao zonse.
11. Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama.
12. Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israyeli, kucigono, ku zidikha za Moabu, ziri ku Yordano pafupi pa Yeriko.