Numeri 3:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Sendera nalo kuno pfuko la Levi, ndi kuwaika pamaso pa Aroni wansembe, kuti amtumikire.

7. Ndipo azisunga udikiro wace, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la cihema cokomanako, kucita nchito ya kacisi.

8. Ndipo asunge zipangizo zonse za cihema cokomanako, ndi udikiro wa ana a Israyeli, kuicita nchito ya kacisi.

9. Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ace amuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ocokera kwa ana a Israyeli.

10. Koma uike Aroni ndi ana ace amuna, azisunga nchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe.

Numeri 3