Numeri 3:19-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndi ana a Kohati monga mwa mabanja ao: Amiramu ndi lzara, Hebroni ndi Uziyeli.

20. Ndi ana a Merari monga mwa mabanja ao: Mali ndi Musi. Awa ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.

21. Banja la Libini, ndi mabanja a Simei, ndiwo a Gerisoni; ndiwo mabanja a Gerisoni.

22. Owerengedwa ao, powawerenga amuna onse, kuyambira mwana wa mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.

23. Mabanja a Agerisoni azimanga mahema ao pambuyo pa kacisi kumadzulo.

24. Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo a Agerisoni ndiye Eliyasafe mwana wa Layeli.

25. Ndipo udikiro wa ana a Gerisoni m'cihema cokomanako ndiwo kacisi, ndi cihema, cophimba cace, ndi nsaru yotsekera pa khomo la cihema cokomanako,

Numeri 3