1. Mibadwo ya Aroni ndi Mose, tsiku lija Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi iyo.
2. Ndipo maina ao a ana amuna a Aroni ndi awa: Woyamba Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
3. Awa ndi maina a ana amuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao acite nchito ya nsembe.