3. Pamenepo ananena fanizo lace, nati,Balamu mwana wa Beori anenetsa,Ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa;
4. Wakumva mau a Mulungu anenetsa,Wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,Wakugwa pansi maso ace openyuka:
5. Ha! mahema ako ngokoma, Yakobo;Zokhalamo zako, Israyeli!
6. Ziyalika monga zigwa,Monga minda m'mphepete mwanyanja,Monga khonje waoka Yehova,Monga mikungudza m'mphepete mwa madzi.
7. Madzi adzayenda naturuka m'zotungira zace,Ndi mbeu zace zidzakhala ku madzi ambiri,Ndi mfumu yace idzamveka koposa Agagi,Ndi ufumu wace udzamveketsa.