30. Ndipo buru anati kwa Balamu, Si ndine buru wako amene umayenda wokwera pa ine ciyambire ndiri wako kufikira lero lino? Kodi ndikakucitira cotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai.
31. Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola liri kudzanja, ndipo anawerama mutu wace, nagwa nkhope yace pansi.
32. Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji buru wako katatu tsopano? taona, ndaturuka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa camtu pamaso panga;
33. koma buru anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.
34. Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndacimwa, popeza sindinadziwa kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati cikuipirani, ndibwerera.