9. Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu ali yense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo.
10. Pamenepo ana a Israyeli anayenda ulendo, namanga mahema m'Oboti.
11. Ndipo anacoka ku Oboti, namanga mahema ku Iyebarimu, m'cipululu cakuno ca Moabu, koturukira dzuwa.
12. Pocokapo anayenda ulendo, namanga mahema m'cigwa ca Zaredi.
13. Atacokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya tina la Arinoni, wokhala m'cipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Moabu, pakati pa Moabu ndi Aamori.