12. Pocokapo anayenda ulendo, namanga mahema m'cigwa ca Zaredi.
13. Atacokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya tina la Arinoni, wokhala m'cipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Moabu, pakati pa Moabu ndi Aamori.
14. Cifukwa cace, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova,Vahebi m'Sufa,Ndi miyendo ya Arinoni;
15. Ndi zigwa za miyendoyoZakutsikira kwao kwa Ari,Ndi kuyandikizana ndi malire a Moabu.
16. Ndipo atacokapo anamuka ku Been, ndico citsime cimene Yehova anacinena kwa Mose, Sonkhanitsa anthu, ndipo ndidzawapatsa madzi.
17. Pamenepo Israyeli anayimba nyimbo iyi:Tumphuka citsime iwe; mucithirire mang'ombe;