Numeri 20:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pamenepo Mose anatumiza amithenga ocokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israyeli, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera;

15. kuti makolo athu anatsikira kumka ku Aigupto, ndipo tinakhala m'Aigupto masiku ambiri; ndipo Aaigupto anacitira zoipa ife, ndi makolo athu.

16. Pamenepo tinapfuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natiturutsa m'Aigupto; ndipo, taonani, tiri m'Kadesi, ndiwo mudzi wa malekezero a malire anu.

17. Tipitetu pakati pa dziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wacifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.

18. Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingaturuke kukomana nawe ndi lupanga.

19. Ndipo ana a Israyeli ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wace; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira.

20. Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anaturukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu.

Numeri 20