33. Koma sanawerenga Alevi mwa ana a Israyeli; monga Yehova adauza Mose.
34. Ndipo ana a Israyeli anacita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ace, monga mwa nyumba za makolo ace.