20. Ndipo oyandikizana naye ndiwo a pfuko la Manase; ndi kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliyeli mwana wa Pedazuri.
21. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.
22. Ndi pfuko la Benjamini: kalonga wa ana a Benjamini ndiye Abidana mwana wa Gideoni.
23. Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.
24. Owerengedwa onse a cigono ca Efraimu ndiwo zikwi makumi khumi mphambu zisanu ndi zitatu kudza zana limodzi, monga mwa makamu ao. Iwo ndiwo aziyenda gulu lacitatu paulendo.