1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
2. Ana a Israyeli azimanga mahema ao yense ku mbendera yace, ya cizindikilo ca nyumba ya kholo lace; amange mahema ao popenyana ndi cihema cokomanako pozungulira.
3. Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa koturuka dzuwa ndiwo a mbendera ya cigono ca Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Yuda ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu.