6. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebi mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zobvala zao;
7. nanena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, nati, Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu.
8. Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m'dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.
9. Cokhaci musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawacokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.
10. Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala, Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'cihema cokomanako kwa ana onse a Israyeli.
11. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, cinkana zizindikilo zonse ndinazicita pakati pao?