Numeri 12:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la cihema, naitana Aroni ndi Miriamu; naturuka onse awiri.

6. Ndipo anati, Tamvani tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.

7. Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m'nyumba mwanga monse.

8. Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, maonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.

9. Pamenepo Mulungu anawapsera mtima iwo; nawacokera iye.

Numeri 12