5. Tikumbukira nsomba tinazidya m'Aigupto cabe, mankaka, ndi mavwendi, ndi anyesi a mitundu itatu;
6. koma tsopano moyo wathu waphwa; tiribe kanthu pamaso pathu koma mana awa.
7. Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ace ngati maonekedwe a bedola.
8. Anthu amamka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.
9. Ndipo pakugwa mame pacigono usiku, mana anagwapo.