31. Koma anati, Usatisiyetu; popeza udziwa poyenera kumanga ife m'cipululu, ndipo udzakhala maso athu.
32. Ndipo kudzatero, ukamuka nafe, inde, kudzali kuti zokoma ziri zonse Yehova aticitira ife, zomwezo tidzakucitira iwe.
33. Ndipo anayenda kucokera ku phiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la cipangano ca Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.