63. Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hokozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgileadi, nachedwa ndi dzina lao.
64. Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa cibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawacotsa ku nchito ya nsembe.
65. Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulikitsa, mpaka wauka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.
66. Msonkhano wonse pamodzi ndiwo zikwi makumi anai ndi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi,