Nehemiya 4:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Tobiya M-amoni anali naye, nati, Cinkana ici acimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala.

4. Imvani, Mulungu wathu, popeza tanyozeka ife; muwabwezere citonzo cao pamtu pao, ndi kuwapereka akhale cofunkhidwa m'dziko la ndende;

5. ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga.

6. Koma tinamanga lingali, ndi linga lonse linalumikizana kufikira pakati mpakati; popeza mitima ya anthu inalunjika kunchito.

7. Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwace munayamba kutsekeka, cidawaipira kwambiri;

8. napangana ciwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kucita cisokonezo m'menemo.

9. Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, cifukwa ca iwowa.

Nehemiya 4