1. Pamenepo Eliasibu mkuru wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ace ansembe, namanga cipata cankhosa; anacipatula, naika zitseko zace, inde anacipatula mpaka nsanja ya Mea, mpaka nsanja ya Hananeeli.
2. Ndi pambali pace anamanga amuna a ku Yeriko. Ndi pambali pao anamanga Zakuri mwana wa Imri.
3. Ndi cipata cansomba anacimanga ana a Hasenaa; anamanga mitanda yace, ndi kuika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipingiridzo yace.
4. Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uliya, mwana wa Kozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana.
5. Ndi pambali pao anakonza Atekoa; koma omveka ao sanapereka makosi ao ku nchito ya Mbuye wao.
6. Ndi cipata cakale anacikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeya anamanga mitanda yace, ndi kuika zitseko zace, ndi zokowera zace, ndi mipingiridzo yace.
7. Ndi pambali pao anakonza Melatiya Mgibeoni, ndi Yadoni Mheronoti, ndi amuna a ku Gibeoni, ndi a ku Mizipa, wa ulamuliro wa ciwanga tsidya lino la mtsinje.