45. Ndipo iwo anasunga udikiro wa Mulungu wao, ndi udikiro wa mayeretsedwe; momwemonso oyimbira ndi odikira, monga mwa lamulo la Davide ndi la Solomo mwana wace.
46. Pakuti m'masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkuru wa oyimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu.
47. Ndi Aisrayeli onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oyimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.