28. Ana a oyimbirawo anasonkhana ocokera ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku midzi ya Anetofati,
29. ndi ku Betegiligala, ndi ku minda ya Geba ndi Azimaveti; popeza oyimbirawo adadzimangira midzi pozungulira Yerusalemu.
30. Ndipo ansembe ndi Alevi anadziyeretsa okha, nayeretsa anthu, ndi zipata, ndi linga.
31. Pamenepo ndinakwera nao akuru a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akuru oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kumka ku cipata ca kudzala;
32. ndi pambuyo pao anayenda Hosaya, ndi limodzi la magawo awiri a akuru a Yuda,
33. ndi Azariya, Ezara ndi Mesulamu,
34. Yuda, ndi Benjamini, ndi Semaya, ndi Yeremiya,
35. ndi ana ena a ansembe ndi malipenga: Zekariya mwana wa Yonatani, mwana wa Semaya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu,
36. ndi abale ace: Semaya, ndi Azareli, Milalai, Gilelai, Maai, Netaneli, ndi Yuda, Hanani, ndi zoyimbira za Davide munthu wa Mulungu; ndi Ezara mlembiyo anawatsogolera;