13. Koma tsopano ndidzatyola ndi kukucotsera goli lace, ndipo ndidzadula zomangira zako.
14. Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m'nyumba ya milungu yako ndidzacotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka.
15. Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! cita madyerero ako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda paceyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse.