3. Ici ndi coipa m'zonse zicitidwa pansi pano, cakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udio, ndipo misala iri m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.
4. Pakuti woyang'ana ndi amoyo onse ali naco ciyembekezo; pakuti garu wamoyo aposa mkango wakufa.
5. Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.
6. Cikondi cao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kali konse kacitidwa pansi pano.
7. Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wabvomerezeratu zocita zako.
8. Zobvala zako zikhale zoyera masiku onse; mutu wako usasowe mafuta.
9. Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wacabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse acabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'nchito zimene ubvutika nazo pansi pano.
10. Ciri conse dzanja lako licipeza kucicita, ucicite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe nchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.