6. Usalole m'kamwa mwako mucimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako cifukwa ninji, naononge nchito ya manja ako?
7. Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zacabe motero mocuruka mau; koma dziopa Mulungu.
8. Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kucotsa cilungamo ndi ciweruzo mwaciwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkuru wopambana asamalira; ndipo alipo akuru ena oposa amenewo.
9. Phindutu la dziko lipindulira onse; ngakhale mfumu munda umthandiza.
10. Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda cuma sadzakhuta phindu; icinso ndi cabe.