13. Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo.
14. Pakuti aturuka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lace asauka.
15. Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, waciwiri, amene adzalowa m'malo mwace.
16. Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m'mbuyo sadzakondwera naye. Icinso ndi cabe nicisautsa mtima.