Mlaliki 10:18-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Tsindwi litewa ndi mphwai za eni ace; nyumba nidontha ndi ulesi wa manja.

19. Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zibvomera zonse.

20. Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'cipinda cogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo couluka ndi mapiko cidzamveketsa zonenazo.

Mlaliki 10