Miyambi 30:13-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Pali mbadwo wokwezatu maso ao,Zikope zao ndi kutukula.

14. Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni;Kuti adye osauka kuwacotsa kudziko, ndi aumphawi kuwacotsa mwa anthu.

15. Msundu uli ndi ana akazi awiri ati, Patsa, patsa,Pali zinthu zitatu sizikhuta konse,Ngakhale zinai sizinena, Kwatha:

16. Manda, ndi cumba,Dziko losakhuta madzi,Ndi moto wosanena, Kwatha.

17. Diso locitira atate wace ciphwete, ndi kunyoza kumvera amace,Makungubwi a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya,

Miyambi 30