Miyambi 15:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo;Koma mau owawitsa aputa msunamo.

2. Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa;Koma m'kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.

3. Maso a Yehova ali ponseponse,Nayang'anira oipa ndi abwino.

Miyambi 15