Miyambi 10:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Amayesa wolungama wodala pamkumbukira;Koma dzina la oipa lidzabvunda.

8. Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo;Koma citsiru colongolola cidzagwa.

9. Woyenda moongoka amayenda osatekeseka;Koma wokhotetsa njira zace adzadziwika.

10. Wotsinzinira acititsa cisoni;Koma wodzudzula momveka acita mtendere.

11. M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo;Koma m'kamwa mwa oipa mubisa ciwawa.

12. Udani upikisanitsa;Koma cikondi cikwirira zolakwa zonse.

13. Nzeru ipezedwa m'milomo ya wozindikira;Koma wopusa pamsana pace ntyole.

14. Anzeru akundika zomwe adziwaKoma m'kamwa mwa citsiru muononga tsopano lino.

15. Cuma ca wolemera ndi mudzi wace wolimba;Koma umphawi wao uononga osauka.

16. Nchito za wolungama zipatsa moyo;Koma phindu la oipa licimwitsa.

Miyambi 10