Miyambi 10:25-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Monga kabvumvulu angopita, momwemo woipa kuti zi;Koma olungama ndiwo maziko osatha.

26. Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso,Momwemo wolesi kwa iwo amene amtuma.

27. Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku;Koma zaka za oipa zidzafinimpha,

28. Ciyembekezo ca olungama ndico cimwemwe;Koma cidikiro ca oipa cidzaonongeka.

29. Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima;Koma akucita zoipa adzaonongeka.

30. Wolungama sadzacotsedwa konse:Koma oipa sadzakhalabe m'dziko.

31. M'kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru;Koma lilime lokhota lidzadulidwa.

32. Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa;Koma m'kamwa mwa oipa munena zokhota,

Miyambi 10